Apolisi akakamizika kufukula mitembo

Apolisi akakamizika kufukula mitembo
Share

Olemba; Kondanani Chilimunthaka

Lachiwiri pa March 10,2020, kunali zodabwitsa ku Zolozolo mu mzinda wa Mzuzu pomwe anamfedwa adapempha kufukulidwa kwa mitembo ya abale awo amwe adayikidwa mmanda sabata lapitali pofuna kuti akayikidwe kwawo ku Mzimba.

Malinga ndizomwe mtolankhani uno wapeza, omwaliwa adali anyamata omwe amkaphunzira pa sukulu ya sekondale ya Masasa mu mzinda wa Mzuzu ndipo adamwalira pangozi ya njinga yamoto yomwe idaombana ndi galimoto masabata awiri apitawo.

Mitembo yawo itasungodwa ku chipatala Cha Mzuzu kwa sabata achipatala mogwirizana ndi apolisi adalamula akayidi kukayika matupiwa koma patapita sabata chiyikireni matupiwa abale adazindikira kuchokera ku Mzimba ndipo adasatira ku Mzuzu ndikuwumiliza a polisi kukafukula mandawo. Izi zidapangitsa kuti Manda okwanira asanu ndi awiri(7) afukulidwe pofuna kuyesayesa kuzindikira pomwe adagonekedwa abale awo.

Pomwe timkalemba nkhaniyi mkuti dongosolo likuchitika kuti atengere mitemboyi kumudzi kwawo ku Mzimba komwe amayembekezera kukachita mwambo wa Maliro.

Malawi Exclusive

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *