Nkhalango ya Viphya ndi Mgodi

Nkhalango ya Viphya ndi Mgodi
Share

Nkhalango ya Viphya ndi Mgodi

Kwa anthu omwe sadayendeko nsewu wa pakati pa Mzuzu ndi Kasungu akamva za nkhalango ya Viphya amangoganiza za mitengo ndi udzu, makamaka mitengo ya payini. Komatu nkhalangoyi muliso mitengo ya bulugama ndi inaso ya chilengedwe.

Koma nkhalango ya Viphya yomwe imadziwika kwambiri kuti Chikangawa ndi Mgodi kwa anthu okhala mozungulira nkhalangoyi ndipo ndi gwelo la chuma komaso, ntchito komaso thandizo la tsiku ndi tsiku kwa mzikazi.

Mwa chitsanzo nkhalango ya Viphya mumapezeka masuku, bowa, ngumbi komanso nkhuni zomwe anthuwa amagulitsa kwa anthu odutsa nseu wa M1 pakati pa Mzuzu ndi Kasungu.

Kudutsa nsewu wa Mzuzu/Kasungu mukangochoka pa chipata Cha Raiply pa ulendo opita ku Kasungu m’mbali mwa nseu mumakhala motanganidwa ndi anthu ogulitsa komaso ogula malondawa.

Komatu awa sitinganene kuti ndiwo adali masomphenya a Ngwazi pokhazikitsa nkhalango ya Viphya yomwe ili ndi mahekitala oposa 42,000, koma lero masomphenya omwe adalipo apherezeraso mu thandizo la tsiku ndi tsiku kwa mzika zokhala mozungulira nkhalangoyi. Bowa komaso masuku ambiri omwe amapezeka mu mzinda wa Mzuzu zimachokera mu nkhalango ya Chikangawa.

Nkhalangoyitu ndi maziko a nyumba zambiri zomwe zamangidwa mdziko muno poti pafupifupi 75% ya matabwa omangira zinthu zosiyanasiyana amachokera mu nkhalango ya Viphya.

Enaso akuphamo nyama mu nkhalangoyi. Malinga ndi kafukufuku yemwe chilimunthaka wachita anthu ambiri akusimba lokoma ndi nkhalango ya Viphya ponena kuti mavuto awo ena amayankhidwa ndi nkhalangoyi.

Komatu ngakhale zili chonchi nkhalango ya Viphya ikukumana ndi zovuta zambiri monga moto olusa Chaka ndi Chaka zomwe zingachepetse mwayi oti anthu azipeza zofunikira mu nkhalangoyi.

Chofunikatu chachikulu mkusamalira nkhalangoyi ngati a Malawi ozungulira nkhalango ya Viphya apitilirebe kusimba lokoma. Kupanda kutero masuku ndi bowa zomwe zasanduka golide wofukulidwa mu nkhalango ya Viphya zikhala mbiri chabe posachedwapa ndipo zidzapangitsa anthu ambiri kukhala opanda ntchito kutha kwa mgodiwu, kwinaku kudzakhalaso kovuta kuti mibadyo ya mtsogolo idzadziwe za masuku ndi bowa.

Ambiri omwe akupeza ntchito mu mgodiwu ndi amayi, ana ndi achinyamata.

Malawi Exclusive

4 thoughts on “Nkhalango ya Viphya ndi Mgodi

  1. 484719 51059Extremely very good written write-up. It will be helpful to anybody who usess it, including myself. Keep up the good work – canr wait to read more posts. 710353

  2. 913466 175672Write more, thats all I have to say. Literally, it seems as though you relied on the video to make your point. You clearly know what youre talking about, why waste your intelligence on just posting videos to your blog when you could be giving us something informative to read? 97002

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *